عن أنس بن مالك قال: قال رسول الله صلى الله عليه وسلم: من ذكرت عنده فليصل علي فإنه من صلى علي مرة صلي عليه عشرا (المعجم الأوسط للطبراني، الرقم: 2767، ورجاله رجال الصحيح كما في القول البديع صـ 237)
Olemekezeka Anas bin Maalik (radhiyallahu anhu) akufotokoza kuti Mtumiki (sallallahu alaih wasallam) adati: yemwe pamaso pake dzina langa latchuridwa, akuyenera kundipangira Durood, chifukwa ndithudi munthu amene angandifunire zabwino kamodzi, Allah adzampatsa madalitso okwana khumi (10).
Kupulumuka kuzinyama zamtchire
Zanenedwa zokhudza shaikh Abul Hassan Shaazlii kuti tsiku linalake adali mkhalango komwe zinyama zamtchire zidayamba kubwera pafupi ndi iye, atagwidwa ndi mantha Kuopa kuti zimuluma, mwachanguchangu adayamba kuwerenga Durood kumfunira zabwino Mtumiki (sallallahu alaih wasallam).
Adachita zimenezi chifukwa zanenedwa mmahadith odziwika bwino omwe akunena zoti, amene angapange Durood kamodzi Allah amampatsa zifundo zokwana khumi 10 ndipo Allah akamuchitira chifundo munthu amamuteteza ku mavuto ena aliwonse, kotero shaikh Shaazlii (rahimahullah) adapulumutsidwa kuzinyama zolusa. (Al Qawlul Badee, Pg, 265)