Kasambidwe Ka Sunnah-Gawo 4

14. Onetsetsani kuti madzi akufika pena paliponse pathupi lanu, nthawi ina iliyonse mukadzithira madzi dzinyureni ndicholinga chofuna kuonetsetsa kuti madziwo alowa pakhungu lonse, ngakhale kutangotsala malo ochepetsetsa kwambiri osathiridwa madzi, kusamba (kwa fardh) sikudzatheka, pamene mukusambitsa thupi, sambitsani kutsogolo kwake kenako kumbuyo.

Read More »

Kufunika kokhala ndi chikhulupiliro chenicheni (choyenera)

Chipembedzo chachisilamu pamodzi ndi nsanamira zake chagona pa chikhulupiliro chenicheni, ngati zikhulupiliro za munthu ndizolakwika, ngakhale kuti sizingamutulutse m’chisilamu, ngakhale atachita ntchito zabwino zachisilamu, sangalandire malipiro amene Allah adalonjeza, chifukwa choti zikhulupiliro zake ndi tsinde lenileni lachisilamu ndizolakwika.

Read More »

Kasambidwe Ka Sunnah-Gawo 3

9. Pangani wudhu onse.

Sayyidatuna Aaishah (radhiyallahu anha) akunena kuti, Mtumiki (sallallahu alaih wasallam) ankati akamakasamba (kusamba kwa fardh) ankayamba ndikusamba m’manja asanalowetse manjawo m’madzi, kenaka ankatsuka malo obisika kenaka ankapanga wudhu ngati m’mene ankapangira(wudhu) akafuna kuswali.

Read More »

Kufika Kwa Durood Ya Ummah Kwa Sayyiduna Rasulullaah (Sallallahu Alaih Wasallam)

Abu Hurairah (radhiyallahu anhu) akusimba kuti Rasulullah (sallallahu alaih wasallam) adanena kuti " nyumba zanu musazipange kukhala ngati ndi manda (zipangeni nyumba zanu kukhala za moyo popangilamo ntchito za bwino monga ngati swalah, kuwerenga Qur’aan majeed ndi zina zambiri. Choncho mukamatero nyumba zanu sizikhala ngati ndi manda kumene sikumachitikako ma aamaal abwino.) Ndipo manda anga musawatenge ngati ndi malo opangilapo zisangalalo, komanso mudziwerenga durood kwa ine, ndithudi mwa njira ina iliyonse Durood yo imandifika (kudzera mwa angelo) kuchokera kwina kuli konse komwe muli."

Read More »

Njira Ya Sunnah Yopangira Wudhu Gawo La chisanu Nchinayi

25. Ngati mbali iliyonse yachiwalo chomwe ndi fardh kusambitsa pamene mukupanga wudhu yasiidwa osasambitsa, wudhu udzakhala opelewera.

Sayyiduna Umar (radhwiyallahu anhu) akunena kuti munthu anapanga wudhu nasiya malo amodzi osasambitsa kuphanzi kwake mlingo wachikhadabu poyang’anitsitsa malo amenewo Mtumiki (sallallahu alaih wasallam) anamuuza iye kuti “pita ukamalizitse kupanga wudhu wako.”

 

Read More »