Ma Ubwino A Wudhu

1. Wudhu ndi chiyeretso chamachimo ang’ono ang’ono.

Sayyiduna Uthmaan (radhwiyallahu anhu) akuti; Mtumiki (sallallahu alaih wasallam) adati: Amene angachite-wudhu, ndipo nawuchita wudhuwo mkachitidwe kabwino kwambiri, Machimo ake (ang´onoang´ono) amafudutidwa (ndipo amatsukidwa) kuchokera mthupi mwake mpakana amagwa machimo kudzera pansi pa-zikhadabo.

Read More »

Kulandila Mphotho Zokwana Makumi Asanu Ndi Ziwiri

Sayyiduna Abdullah bin Amr bin Aas (radhwiyallahu anhuma) akufotokoza kuti, munthu amene angamfunile zabwino Nabi (sallallahu alaih wasallam) kamodzi, Allah amanchitira chisoni munthu ameneyo kokwana ka 70, angelo amamupemphera chisoni munthu ameneyo kokwana ka 70 komanso ndi madalitso kukhala ngati malipilo a kumfunila mtumiki zabwino kamodzi. Choncho munthu amene akufuna kuti achulukitse kumfunila zabwino Nabi (sallallahu alaih wasallam) ayenera kutero, komanso amene akufuna kuti achepetse akhonzanso kutero (ngati akufuna kuti apeze malipilo ochuluka akuyenera kuchulukitsa kumfunila zabwino Nabiiyo).

Read More »

Masaail (Nfundo) Zina Zokhudza Kuzithandiza Kuchimbudzi

1. Funso: kodi ndizoloredwa munthu kuwerenga mabukhu monga nyuzi ndi magazini, kapena kugwiritsa ntchito foni, kapenanso kuseweretsa intaneti pamene ali m’nchimbudzi?

Yankho: Chimbudzi ndi malo amene munthu amazithandizirako, Choncho sizabwino kwa munthu kugwiritsa ntchito foni yake kapena kuwerenga uthenga uliwonse kapena kuwerenga nkhani m'nchimbudzi.

Read More »

Kupeza Sawabu Zomasura Akapolo Okwana Khumi (10)

Sayyiduna Baraa bin Aazib (radhwiyallahu anhu) akunena kuti Nabi (sallallahu alaih wasallam) adati, "amene angandiwelengere Durood kamodzi, mmalo mwa Durood imeneyo Allah adzamulipira munthu ameneyo sawabu zokwana khumi adzamufufutira (adzamukhululukira) machimo okwana khumi adzamukwezera ulemelero wake ndimasiteji khumi komanso Durood yomwe adawerengayo idzakhala njira yomupatsa sawabu zomasura akapolo khumi.

Read More »

Kukhululukidwa Machimo

Sayyiduna Abu Burdah (radhwiyallahu anhu) akusimba kuti, Nabi (sallallahu alaih wasallam) adati,” amene anganditumizire Durood mwa ummah wanga kuchokera pansi pa mtima, Allah adzamdalitsa munthu ameneyo pompatsa zifundo zokwana khumi, adzamukwezera ulemelero wake ndi masiteji okwana khumi ku Jannah, adzamulipira sawabu zokwana khumi ndikumukhululukira machimo okwana khumi.”

Read More »

Kapangidwe Ka Istinja (Kutawasa) Ka Sunnah ~ Gawo Lachisanu

16. Dzithandizeni mutanjuta pansi, ndi makuruhu (zonyasa) kudzithandiza choima.[1] عن عائشة رضي الله عنها قالت من حدثكم أن النبي صلى الله عليه وسلم كان يبول قائما فلا تصدقوه ما كان يبول إلا قاعدا (سنن الترمذي، الرقم: 12)[2] Sayyiduna Aishah (radhwiyallahu anha) akuti, amene angakuuzeni kuti Nabi (sallallahu alaih wasallam) ankadzithandiza …

Read More »