admin

Kuwolowa manja ndi Zuhd (Kudzipatula padziko lapansi) kwa Abu Ubaidah (Radhwiyallahu ‘anhu)

Nthawi ina, Umar (Radhwiya Allahu ‘anhu) adatenga ndalama za golide mazana anayi, naziika m’thumba napereka kwa wantchito wake: “Pita kwa Abu Ubaidah (Radhwiyallahu ‘anhu) ndipo ukampatse ndalamazi. Ukakafika kumeneko ukadikire kwa kanthawi kuti ukawone zomwe akachite ndi ndalamazo (ndipo ukabwerere ndikundidziwitsa).” Kapoloyo anatenga thumba la ndalama za golide lija napita …

Read More »

Ma Sunnah Komanso Miyambo Ya Dua 1

1. Yambani dua pomulemekeza Allah kenako mudzamuwerengera duruud Mtumiki (Swallallahu alaihi wasallam). Pambuyo pake, modzichepetsa ndi ulemu onse, mudzapempha zosowa zanu pamaso pa Allah. Olemekezeka Fadhaalah bin Ubaid (Radhwiyallahu anhu) akusimba kuti nthawi ina Rasulullah (Swallallahu alaihi wasallam) adakhala munzikiti pamene munthu wina adalowa ndikuyamba kuswali. Kenako adapempha nati: “Oh, …

Read More »

Abu Ubaidah (Radhwiyallahu ‘anhu) aluza mano ake pa nkhondo ya Uhud

Pankhondo ya Uhud, Rasulullah (Swalla Allaahu ‘alayhi wasallam) adamenyedwa koopsa ndi adani ndipo mano awiri a chisoti chake chachitsulo chovala pankhondo adalowa mmatsaya ake odalitsika. Abu Bakr Siddiiq (Radhwiyallahu ‘anhu) ndi Abu Ubaidah (Radhwiyallahu ‘anhu) nthawi yomweyo anathamanga kukamuthandiza Mtumiki (Swalla Allaahu ‘alayhi wasallam). Abu Ubaidah (Radhwiyallahu ‘anhu) anayamba kuzula …

Read More »

Kodi Amaanah Imatanthauza Chiyani?

Amaanah imatanthauza kuti munthu akhale olingalira za tsiku lachiweruzo pamene adzaime pamaso pa Allah pankhani ya maudindo amene munthu ali nawo kwa Allah ndi akapolo a Allah. Limeneri ndi khalidwe labwino kwambiri kotero kuti ndi khomo lopezera zabwino zosawerengeka za uzimu ndi thupi zochoka kwa Allah. Ubwino wa amaanah umapanga …

Read More »

Nthawi Zomwe Ma Dua Amayankhidwa

Nthawi ya Azaan ndi Pamene Magulu Awiri Akumana Pankhondo Olemekezeka Sahl bin Sa’d (Radhwiyallahu anhu) akusimba kuti Mtumiki (Swallallah alaihi wasallam) adati: “Pali nthawi ziwiri zomwe madua sangakanidwe kapena nthawi zambiri sangapande osayankhidwa; pa nthawi ya Azaan ndi pamene magulu awiri ankhondo akumana pankhondo.”[1] Pakati pa Azaan ndi Iqaamah Olemekezeka …

Read More »

Khumbo la Umar (Radhwiyallahu ‘anhu) kudalitsidwa ndi Chipinda Chodzaza ndi Anthu monga Abu Ubaidah (radhiyallahu ‘anhu)

Umar (Radhwiyallahu ‘anhu) nthawi ina anakhala pansi ndi gulu la maswahabah pamene iye analankhula nawo ndipo kenako anafunsa funso lonena kuti, “Tandiuzani chimene anthu inu mukulakalaka” Munthu wina adati: “Chokhumba chomwe ndili nacho ndikuti chipinda chonsechi chitadzadza ndi ma dirham (ndalama zasiliva) ndikuti ndiwononge zonsezo panjira ya Allah Ta’ala.” Umar …

Read More »

Anthu Omwe Ma Duwa Awo Amayankhidwa 3

Munthu Wachikulire Okhala ndi invi Olemekezeka Anas (Radhwiyallahu anhu) akusimba kuti Mtumiki (Swallallahu alaihi wasallam) adati: “Ndithu Allah amachita manyazi kukana duwa ya munthu (okalamba) watsitsi loyera ngati ali olungama Munthu Opanga Dua Pagulu Olemekezeka Habiib bun Maslamah (Radhwiyallahu anhu) akusimba kuti Mtumiki (Swallallahu alaihi wasallam) adati: “Palibe gulu la …

Read More »

Kudalirika Kwenikweni Kwa Olemekezeka Abu Ubaidah bin Jarrah (Radhwiyallahu ‘anhu)

Anthu a ku Najraan atalowa Chisilamu, adadza kwa Mtumiki (Swalla Allaahu ‘alayhi wasallam) namupempha kuti awatumizire munthu odalirika (yemwe angakawaphunzitse Swalah). Mtumiki (Swalla Allaahu ‘alayhi wasallam) adati kwa iwo: لأبعثن إليكم رجلا أمينا حق أمين Ndidzatumizirani munthu okhulupirira ndi odalirika kwambiri. Pa nthawiyo, ma Swabsaabah (Radhwiyallahu anhum) omwe adalipo onse …

Read More »

Anthu Omwe Ma Duwa Awo Amayankhidwa 2

Munthu Yemwe Akudwala Olemekezeka Umar (Radhwiyallahu anahu) akusimba kuti Mtumiki (Swallallahu alaihi wasallam) adati: “Mukakumana ndi odwala, mupempheni kuti akupangireni duwa chifukwa dua yake ili ngati dua ya angero (chifukwa cha kudwalako, machimo ake amakhululukidwa), choncho akufanana ndi angelo pokhala opanda machimo, ndipo potero pempho lake lidzalandiridwa mwachangu). Yemwe Amapanga …

Read More »