Kuthetsa Umphawi

Sayyiduna Samurah Suwaai (radhwiyallahu anhu), bambo a Jaabir radhwiyallahu anhu akufotokoza kuti, tsiku lina tidali pamodzi ndi Mtumiki (sallallahu alaih wasallam) ndipo kudabwera munthu wina namufunsa Mtumiki (sallallahu alaihi wasallam) kuti, oh Mtumiki wa Allah (sallallahu alaihi wasallam), ndi ntchito (ibadah) iti yomwe ndi yokondedwa kwambiri pamaso pa Allah? 

Read More »

Kuikonzekera Ramadhan

8. Pamene Ramadhan ikubwera komanso tili mkati kati mwa Ramadhan yesetsani kumanena dua yotsatirayi: اَللّٰهُمَّ سَلِّمْنِيْ لِرَمَضَانَ وَسَلِّمْ رَمَضَانَ لِيْ وَسَلِّمْهُ لِيْ مُتَقَبَّلًا O Allaah nditetezeni ine pondifikitsa m’mwezi wa Ramadhan (ndili wa thanzi komanso nyonga ndicholinga choti ndipindule kwambiri m’mweziwu) komanso usamaleni mwezi wa Ramadhan kwa ine (poupangitsa kuti …

Read More »

Njira Ya Sunnah Yopangira Wudhu Gawo lachitatu

6. Chukuchani mkamwa ndikuthira madzi mphuno nthawi imodzi katatu. Kachukuchidwe kamkamwa ndikuthira madzi mphuno kali motere, choyamba tengani madzi mdzanja lanu lamanja, kenako, pogwiritsa ntchito madzi ena, tsukani mkamwa kamodzi otsalawo gwiritsani ntchito kutsuka mphuno, mudzabwereza zimenezi kawiri kotsalako pogwiritsa ntchito madzi ena ulendo wina uliwonse.

Read More »

Kuyankhidwa Kwa Ma Duwa

Umar (radhwiyallahu anhu) akulongosora kuti: Duwa imakhala idakali pakati pa mitambo ndi nthaka (munlengalenga). Siimapititsidwa mpakana kumwamba ngati muduwamo simunawerengedwe Durood (kutanthauza kuti sipamakhala chitsimikizo cha kuyankhidwa kwa duwayo).

Read More »

Kuikonzekera Ramadhan 1

1. Ikonzekereni bwino Ramadhan isanayambe, anthu m’mbuyomo ankaukonzekera mwezi umenewu patatsala miyezi isanu ndi umodzi. 2. Mwezi wa Rajab ukayamba mudzwelenga duwa iyi: اَللّٰهُمَّ بَارِكْ لَنَا فِيْ رَجَبٍ وَّشَعْبَان وَبَلِّغْنَا رَمَضَان Oh Allah tidalitseni m’mwezi umenewu wa Rajab ndi Sha’baan, ndipo tiloreni kuti tifike mwezi wa Ramadhan. عن أنسٍ رضي …

Read More »

Njira Ya Sunnah Yopangira Wudhu Gawo lachiwiri

4. Sambitsani m'manja katatu.

Sayyiduna Humraan (rahimahullah) kapolo omasuridwa wa Uthmaan (radhwiyallahu anhu) akusimba kuti: Sayyiduna Uthman (radhwiiyallahu anhu) anapempha madzi (kuti awaonetse anthu kapangidwe ka wudhu. kenaka anayama kupanga wudhu posambitsa manja ake (mpaka molumikizanirana dzanja) katatu (izi zafotokozedwazi zomwe zikupezeka mu sahihul bukhari sayyiduna Uthman (Radhwyallahu anhu) anati: ndidamuona Mtumiki (sallallahu alaihi wasallam) akupanga wudhu motere)."

Read More »

Kupeza Mwayi Okhala Pafupi Ndi Nabi (Salallah Alayhi Wasallam) Patsiku Lachiweruzo

Sayyiduna Abu umaamah (radhwiyallahu anhu) akusimbanso kuti: Nabi (sallallahu alaih wasallam) adati: “Chulukitsani kunditumizira Durood ine lachisanu lililonse, Ndithudi Durood imene ummah wanga umachita imabweretsedwa kwa ine lachisanu lililonse. (Choncho) amene amachulukitsa kunditumizira Durood ineyo ndi amene adzakhale kufupi kwambiri ndi ine (patsiku lachiweruzo).

Read More »