Sayyiduna Umar (radhiyallahu anhu) akusimba kuti, maduwa amatsakamira m’lengalenga. Samadutsa kupita kumwamba ngati durood siikutumizidwa kwa Mtumiki (sallallahu alaih wasallam) (palibe galantidi yoti duwayo ilandiridwa).
Read More »Njira Ya Sunnah Yogwiritsira Ntchito Miswaak (mswachi ochokera ku mtengo)
1. Njira yogwilira miswaak ili motere, Munthu ayenere ayike chala chachikulu ndi chaching´ono pansi pa miswaak ndipo zala zake zotsalazo ayike mbali yapamwamba pa Miswaak.[1] 2. Gwirani Miswaak ndi mkono wamanja ndipo yambani kutsuka mano kuyambira mbali yakumanja.[2] 3. Tsukani mano mopingasa ndipo lilime mulitsuke molitsatira (mulitali make), chimodzimodzinso, tsukani …
Read More »Mmene Allah Taala Amazisamalilira Zolengedwa Zake
6. Chigamulo cha Allah chilichonse muli nzeru ndiluntha ngakhalebe munthu samatha kumvetsa zolinga za Allah Ta'ala. Choncho munthu akuyenera kumvetsa ndi kusangalala ndi Chigamulo cha Allah Ta’ala nthawi zonse.
Read More »Mtumiki (Sallallahu Alaih Wasallam) Kumpemphera Munthu Chikhululuko
Sayyiduna Umar bin Khattwaab (radhiyallahu anhu) akufotokoza kuti Mtumiki (sallallahu alaih wasallam) adati, Chulukitsani kundiwerengera Durood usiku ndi Usana wa tsiku la Jumuah (lachisanu) chifukwa Durood yanuyo imandipeza ndipo ndimakupangirani duwa kukupempherani chikhululuko kwa Allah ku machimo anu.
Read More »Ubwino ogwiritsa ntchito miswak
1. Kugwiritsa ntchito miswak kumaonjezera sawaabu za swalah ka 70.
Sayyiduna Aaishah radhiyallahu anha akunena kuti Mtumiki (sallallahu alaih wasallam) adati, swalah imene yapempheledwa utagwiritsa ntchito miswak (popanga wudhu) ilindi sawaab zokwana 70 kuposa swalah yomwe yaswalidwa popanda kugwiritsa ntchito miswak.
Read More »Mmene Allah Taala Amazisamalilira Zolengedwa Zake
1. Allah Taala ndi wachisoni kwambiri kwa akapolo ake. Ndipo Iye Allah amakonda kwambiri akapolo, wodekha kwa akapolo ake komanso opilira kwambiri. Iye amakhululuka machimo ndiponso amalandila kulapa kwa akapolo ake.[1] 2. Allah Taala ndi mwini chilungamo chonse. Iye sapondereza akapolo ake ngakhale mpang´ono pomwe.[2] 3. Allah Taala anamupatsa munthu …
Read More »Kuwerenga Durood Usiku Ndi Usana Wa Tsiku La Jumuah (Lachisanu)
Sayyiduna Aws bin Aws (radhiyallahu anhu) akusimba kuti Mtumiki (sallallahu alaih wasallam) adati, “tsiku lopambana kwambiri ndi tsiku la Jumuah/lachisanu, kotero, Chulukitsani kundiwerengera durood tsiku limeneli popeza durood yanu imabweretsedwa kwa ine, masahabah adafunsa kuti, “durood yathu idzakufikani bwanji mukadzamwalira poti mafupa anu adzakhala ataola?” Mtumiki (sallallahu alaih wasallam) adayankha nati, “ndithudi Allah adailetsa nthaka kudya matupi a aneneri.”
Read More »Nthawi Zomwe Ndi Sunnah Kusambanthawi Zomwe Ndi Sunnah Kusamba
Pali nthawi zambiri zimene kusamba ndisunnah, zina mwa nthawizi ndi izi:
1.Tsiku la Jumua (lachisanu).
Sayyiduna Abullah bin Umar (radhwiyallahu anhuma) akunena kuti Mtumiki (Sallallahu alaih Wasallam) anati,” pamene wina mwainu akubwera ku swala ya Jumua (lachisanu) ayenera kusamba.”
Read More »Zikhulupiliro zokhudza Allah – 2
6. Palibe chilichonse chofanana ndi Allah Taala mayina ake ndi mbiri zake. Iye ndiokwanilira ulemelero wake ndi mbiri zake, palibe chinachirichonse chofanana ndi Allah Ta'ala mphamvu kapena maonekedwe. Iye Allah Ta'ala alibe maonekedwe kapena mtundu ofanana ndicholengedwa chirichonse.
Read More »Kulandila Satifiketi Yomasuridwa Ku Unaafiq Komanso Ku Moto Wa Jahannam
Sayyiduna Anas (radhiyallahu anhu) akusimba kuti, Mtumiki (sallallahu alaih wasallam) adati, “amene anganditumizire Durood kamodzi ngati malipiro ya Durood Allah adzamulipira munthu ameneyo sawabu ndikumuchitira chifundo ka 10, ndipo amene anganditumizire Durood kokwana ka 10 Allah adzamulipira munthu ameneyo sawabu zokwana 100, ndipo munthu amene anganditumizire Durood kokwana ka 100 Allah adzamulembera chiphaso pakati pa maso ake yommasura ku ukamberembere komanso ku chilango cha Jahannam, Ndiponso Allah adzamulemekeza munthu ameneyo pa tsiku la Qiyaamah pomudzutsa ndi gulu la anthu omwe adafera ku nkhondo”.
Read More »