Monthly Archives: September 2025

Kumasuridwa kwa Hazrat Bilaal (Radhwiya Allaahu ‘anhu) ndi Nabiy (Swalla Allaahu ‘alayhi wa aalihi wasallam) kufuna kuti Hazrat Bilaal (Radhwiyallahu ‘anhu) amasuridwe.

Nthawi ina pamene ankalankhula za Hazrat Bilaal (Radhiyallahu ‘anhu), Hazrat Sa’eed bun Musayyib (rahimahullah) adati: khumbo lofuna kulowa Chisilamu linali lalikulu kwambiri mu mtima mwa Hazrat Bilaal (radhwiyallahu ‘anhu). Adakumana ndi mavuto ndi mazunzo osalekeza kuchokera kwa anthu osakhulupirira. Nthawi zonse anthu osakhulupirira akafuna kumukakamiza kusiya Chisilamu, iye adali kukana …

Read More »

Tafseer Ya Surah Naazi’aat

وَالنَّازِعَاتِ غَرْقًا ‎﴿١﴾‏ وَالنَّاشِطَاتِ نَشْطًا ‎﴿٢﴾‏ وَالسَّابِحَاتِ سَبْحًا ‎﴿٣﴾‏ فَالسَّابِقَاتِ سَبْقًا ‎﴿٤﴾‏ فَالْمُدَبِّرَاتِ أَمْرًا ‎﴿٥﴾ Ndikulumbirira (angelo) amene amachotsa (mizimu ya osakhulupirira) mwaukali, ndi (angelo) amene amachotsa (miyoyo ya okhulupirira) moleza, ndi (Angelo) amene amasambira nayo mizimuyo (m’mlengalenga), ndi (Angelo) amene amapikisana (kukwaniritsa malamulo a Allah Ta’ala). Monga ziliri kuti Sura Nabai idavumbulutsidwa kuti idzakhazikitse chikhulupiriro cha tsiku la …

Read More »

Sunnats Ndi Aadaab Za Salaam 10

30. Popanga musaafah, ingogwirani manja a munthuyo, Palibe chifukwa chogwirana chanza ndikumavinitsa monga amachitira ma kuffaar. Chimodzimodzinso sizoyenera kupanga musaafahah uku ndikumapsopsona dzanja lake ndikumasisita pachifuwa chake popeza machitidwewa alibe maziko mu Dini. 31. Popanga musaafah, musagwire manja a munthu winayo momufinya mpaka kumupweteka. 32. Musafulumire kuchotsa manja anu mukapanga …

Read More »

Olemekezeka Bilaal (Radhwiya Allaahu ‘anhu) achita Azaan ku Shaam

‘Umar (Radhiyallahu ‘anhu) ulendo wina atapita ku Baitul Muqaddas m’nthawi ya Khilaafat yake, adayendera Jaabiyah (malo ena ake ku Shaam). Ali ku Jaabiyah anthu adadza kwa iye ndikumupempha ngati angamupemphe Bilaal (Radhwiyallahu ‘anhu) yemwe ankakhala ku Shaam kuti awachitire azaan chifukwa iye adali muazzin wa Mtumiki (Swalla Allaahu ‘alayhi wa …

Read More »

Sunnats Ndi Aadaab Za Salaam 9

27. Wina asapereke salaamu pomlonjera munthu amene si Msilamu. Ngati amene sali Msilamu apereka moni wa salaamu, ayankhe pongonena kuti “Wa alaik” (ndi pa inu), ndipo ngati ambiri omwe si Asilamu apereka salaam kwa munthu, ayenera kuyankha kuti “Wa alaikum” (ndi kwa inu nonse). 28. Akakumana Asilamu awiri, akamaliza salaam, …

Read More »

Olemekezeka Bilaal (Radhwiya Allaahu ‘anhu) Msungichuma wa Mtumiki (Swalla Allaahu ‘alayhi wa aalihi wasallam)

Olemekezeka Abdullah Al-Hawzani (rahimahullah) akufotokoza kuti nthawi ina adakumana ndi Bilaal (radhwiyallahu ‘anhu) ku Halab (mzinda wa Shaam). Atakumana ndi Bilaal (Radhwiya Allaahu ‘anhu) adamufunsa kuti: “E, Bilaal (Radhwiyallahu ‘anhu)! Ndiuze momwe Nabiy (Swalla Allaahu ‘alayhi wa aalihi wasallam) ankagwiritsira ntchito chuma chake (pa ntchito ya dini). Bilaal (Radhwiya Allaahu …

Read More »

Sunnats Ndi Aadaab Za Salaam 8

26. Ndi adab (makhalidwe a usilamu) kuti pamene munthu wina akuyenda, wina wakhala pansi, ndiye kuti oyendayo ayambe kupereka salaamu ndi kupereka moni. Chimodzimodzinso, pamene wina ali m’sitima yapamadzi ndipo wina akuyenda, ndiye kuti okwerayo ayenera kuyamba kupereka salamu ndi kupereka moni. Chimodzimodzinso, achichepere ayenera kupereka moni kwa akuluakulu, ndipo …

Read More »

Kukhala Ndi Nkhawa Pa Maphunziro A Dini A Mwana

Fuko lodalitsidwa ndi maphunziroo a Dini ndi kumvetsetsa komveka bwino komanso ndi fuko lopita chitsogolo komanso lachitukuko lomwe lili ndi tsogolo labwino. Mbali inayi, mtundu opanda maphunziro a Dini ndi kuzindikira koyenera ndi mtundu omwe ukupita kuchiwonongeko ndi kulephera. Ndichifukwa chake Nabi aliyense akatumizidwa ku fuko linalake, ndiye kuti imodzi …

Read More »

Bilaal (Radhwiya Allaahu ‘anhu) Aitana Azaan pa Ka’bah

Nthawi ya Fath-e-Makkah (Kugonjetsa kwa Makka), Mtumiki (Swalla Allaahu ‘alayhi wasallam) adalowa mu Ka’bah Shariif pamodzi ndi Bilaal (radhwiyallahu ‘anhu) komanso Usaamah (radhwiyallahu ‘anhu). Pa nthawiyo, Mzikiti udali odzadza ndi ma Quraishi omwe adali mmizeremizere, akumuyang’ana Mtumiki (Swalla Allaahu ‘alayhi wa aalihi wasallam) kuti aone zimene achite ndi momwe awachite …

Read More »

Sunnats Ndi Aadaab Za Salaam 7

21. Pamene mukudzithandiza, musapereke salaamu kwa munthu aliyense kapena kuyankha salamu ya munthu aliyense. Chimodzimodzinso, ngati munthu akudzithandiza, musamupatse salaamu. 22. Muyenera kupereka salaamu kwa akulu akulu anu modzichepetsa komaso ndi motsitsa mawu. 23. Ngati mwalonjeza kupereka salaamu ya munthu kwa wina, zimakhala Waajib kwa iwe kukwaniritsa lonjezo ndi kupereka …

Read More »