Zikhulupiliro Zokhudza Angelo

10. Angelo amene amamufunsa munthu mafunso m’manda maina awo ndi Munkar ndi Nakiir.[1] ndipo mafunso omwe amafunsa ndi awa: a) Mbuye wako ndindani? b) Ungatiuze chani chokhuza Muhammad sallallah alaih wasallam? c) Chipembedzo chako ndi chiti?[2] 11. Mnsilamu aliyense ali ndi M’ngelo komanso shaitaan, M’ngelo amamulimbikitsa munthuyo kuchita zabwino ndipo …

Read More »

Nthawi Zimene Miswak Ikufunika Kugwirtsidwa Ntchito

7. Pamene wina ali kumapeto kwa moyo wake (ali pafupi kumwalira).

Sayyidatuna Aisha (radhiyallahu anha) akufotokoza kuti, Mtumiki (sallallahu alaih wasallam) atatsala pang’ono kumwalira nchimwene wanga amene ndi AbdulRahmaan (radhiyallahu anhu) adalowa mchipinda chomwe Mtumiki (sallallah alaih wasallam) adagona atanyamula miswaak yomwe ankagwiritsa ntchito kutsukira mkamwa.

Read More »

Zikhulupiliro Zokhudza Angelo

6. Mikaa’eel (alaihis salaam) ndi amene amayang’anira zachakudya ndi nvula, angelo ena amagwira ntchito pansi pake ndipo amayang’anira mitambo nyanja mitsinje ndi mphepo, amauzidwa zoti achite ndi Allah ndipo kenaka amapeleka uthenga kwa angelo ena omwe ali pambuyo pake. 7. Israafeel (alaihis salaam) amalamuridwa ndi Allah kuti achotse mizimu ya …

Read More »

Munthu Waumbombo

Sayyiduna Husain (radhiyallahu anhu) akufotokoza kuti Mtumiki (sallallahu alaih wasallam) adati, munthu waumbombo kwambiri ndi amene amati akanva dzina langa samandifunira zabwino.

Read More »

Nthawi Zimene Miswak Ikufunika Kugwirtsidwa Ntchito

4. Pamene mukupanga wuzu.

Sayyiduna Abu Hurairah (radhiyallahu anhu) akuakufotokoza kuti Mtumiki (sallallahu alaih Wasalaam) adati, “chikhala kuti sichipsinjo pa ummah wanga ndikadawalamula (ndikadazipanga kukhala zokakamiza) kuti adzigwiritsa ntchito miswaak nthawi inailiyonse pamene akupanga wudhu (komano Sizili zokakamiza kutero koma ndisunnah yomwe yalimbikitsidwa pamene mukupanga wudhu).”

Read More »

Zikhulupiliro Zokhudza Angelo

1. Angelo ndizolengedwa zomwe zilibe tchimo komanso adalengedwa kuchokera mukuwala, angelo samaoneka ndi maso athu, ndipo sii amuna kapena akazi. iwowa samadya kumwa kapena kugona monga amachitira munthu.[1] 2. Allah adawapatsa iwowa maudindo osiyanasiyana, amakwaniritsa lamulo lirilonse limene alamuridwa ndipo samanyozera malamulo a Allah.[2] 3. Sitimadziwa chiwelengero chenicheni cha Angelo …

Read More »

Kuwerenga Durood M’mawa Ndi Madzulo

Sayyiduna Abu Dardaa (radhiyallahu anhu) akufotokoza kuti Mtumiki (sallallahu alaih wasallam) adati, “munthu amene angandifunire zabwino pondiwerengera Durood kokwana ka khumi m’mawa ulionse komanso kumadzulo kulikonse adzapeza nawo pempho langa la Shafaa patsiku lachiweruzo.”

Read More »

Zikhulupiliro Zokhudza Atumiki a Mulungu alaihim Salaam

6. Kuchuluka kwa aneneri onse akudziwa ndi Allah yekha, timakhulupilira mwa atumiki onse angakhale ochuluka bwanji. 7. Monga ziliri kuti ndi chizindikiro cha utumiki, Allah amamulora mtumiki kuchita zodabwitsa zomwe zimatchedwa kuti Mu’ujizaat. Komano Tikuyenera kuzindikira kuti mtumiki ndi munthuso ndipo sangapange zodabwitsa mwa iye yekha, zimangochitika kudzera muchifuniro cha …

Read More »