Sunnah komanso miyambo yoyenera kutsatira usanayambe Kuwerenga Quraan Majiid 9

21. Mukamaliza kuwerenga Qur’an yonse mpaka kukafika Surah Naas, zili mustahab kuti muyambirenso kuwerenga poyambiranso ndi Surah Faatihah ndi aya zoyambira za Surah Baqarah mpaka ulaaika humul muflihuun. 22. Mukamaliza kuwerenga Quraan yonse, werengani dua iyi: اَللّٰهُمَّ ارْحَمْنِيْ بِالْقُرْآنْ وَاجْعَلْهُ لِيْ إِمَاماً وَّهُدًى وَّرَحْمَةً اَللّٰهُمَّ ذَكِّرْنِيْ مِنْهُ مَا نَسِيْتُ وَعَلِّمْنِيْ …

Read More »

Ntchito yabwino yomwe Sa’d (radhiyallahu ‘anhu) adalandira nayo nkhani yabwino yokalowa Jannah

Olemekezeka Anas (radhwiya allaahu ‘anhu) anasimba kuti nthawi ina maSwahaabah (radhwiyallahu anhum) adakhala ndi Mtumiki (swalla allaahu ‘alayhi wasallam) pamene adati: “M’kanthawi kochepa aonekera munthu wa ku Jannah pamaso panu.” Nthawi yomweyo, Sa’d (radhwiyallahu anhu) adatulukira atanyamula nsapato zake kudzanja lake lamanzere, ndevu zake zikuchucha madzi a wudhu. Tsiku lachiwiri …

Read More »

Sunnah komanso miyambo yoyenera kutsatira usanayambe Kuwerenga Quraan Majiid 8

19. Ngati mukufuna kusintha zobvala zanu m’chipinda chosungiramo Quraan Majiid, muyenera kuika kaye Qur’an Majiid m’kabati, m’dilowa ndi zina zotero musanavule. Kuvula pamaso pa Quraan Majiid ndikotsutsana ndi ulemu wa Quraan Majiid. 20.Ngati ukuwerenga ndime ya Sajdah kapena kuimvera ikuwerengedwa, zidzakhala Waajib (zokakamizidwa) kwa iwe kuchita Sajdah. Kapangidwe ka sajdah-e-tilaawat …

Read More »

Zotsutsa za Anthu Ena aku Kufah:

M’chaka cha 21 A.H, anthu ena aku Kufah adadza kwa Umar (radhwiyallahu ‘anhu) ndipo adadandaula za Sa’d (radhwiyallahu ‘anhu) kuti sakumaswalitsa bwino. Nthawi imeneyo, Sa’d (radhwiyallahu anhu) adasankhidwa ndi Umar (radhwiyallahu ‘anhu) kukhala bwanamkubwa waku Kufah. Umar (radhwiyallahu anhu) adamuitana Sa’d (radhwiyallahu ‘anhu) ndipo atafika adalankhula naye mwaulemu nati: “E, …

Read More »

Umoyo Wa Chisilamu

Munthu akamira m’madzi n’kumavutika kuti apulumuke, angachite chilichonse kuti apulumutse moyo wake. Ngati Angakwanitse kugwira chingwe chapafupi chomwe angadzitulutse m’madzimo amachikakamira n’kumachiona ngati ndi njira yake yopulumutsira moyo. M’dziko lino lapansi, M’silamu ngati akakumane ndi mafunde amphamvu a fitnah (mayesero) omwe akupereka chiopsezo chommiza m’machimo ndi kuononga chipembedzo chake, adzifunse …

Read More »

Muvi Oyamba kulasa Mchisilamu

Olemekezeka Sa’d (radhwiyallahu ‘anhu) adali m’gulu la ma Swahaabah omwe Mtumiki (swallallaahu ‘alayhi wasallam) adawatumiza m’chaka choyamba cha Hijrah kuti akalimbane ndi gulu la ma Quraishi Paulendowu, Mtumiki (sawllallahu alaihi wasallam) adamusnkha Sa’ d (radhwiyallahu anhu) kukhala mtsogoleri wa gululi, Pa ulendowu maswahaaba (radhwiyallahu ‘anhum) adapita ku Rabigh komwe adakumana …

Read More »

Sunnah komanso miyambo yoyenera kutsatira usanayambe Kuwerenga Quraan Majiid 6

14. Pamene mwatanganidwa ndi kuwerenga Qur’an Majiid, onetsani chidwi chanu pa Qur’an Majiid. Musatanganidwe ndi zokambirana zapadziko lapansi pakati panu mkatikati mowerenga, makamaka pamene Quraan ili yovundukura. Ngati pakufunika kuyankhula, ndiye kuti mutsirize Aayah yomwe mukuiwerengayo, mutseke Quraan mwaulemu, kenako yankhulani. Zanenedwa kuti Ibnu Umar (radhwiyallahu anhuma) akamawerenga Qur’aan Majiid, …

Read More »

Magazi Oyamba Kukhetsedwa Chifukwa cha Chisilamu

Muhammad bin Ishaaq (rahimahullah) anati: Kumayambiriro kwa Chisilamu, ma Swahaabah a Mtumiki (Swallallaahu ‘alaihi wasallam) ankaswali mobisa. Iwo ankapita kuzigwa za Makka Mukarramah kukaswali kuti Swalaah yawo ikhale yobisika kwa osakhulupirira (ndi kuti apulumuke ku mazunzo a anthu osakhulupirira). Tsiku lina Sa’d (Radhwiyallahu ‘anhu) adali nawo pamodzi ndi gulu la …

Read More »

Chisilamu Chimaitanira Ku Chiyani?

M’nthawi ya Rasulullah swallallahu alaihi wasallam, anthu osiyanasiyana adayamba kulowa Chisilamu. Uthenga wa Chisilamu ukufalikira ndikufikira madera osiyanasiyana, Aksam bin Saifi rahimahullah mtsogoleri wa banja la Tamiim, adakhala ndi chidwi chofuna kudziwa za Chisilamu. Choncho, adatumiza anthu awiri amtundu wake kuti apite ku Madina Munawwarah kuti akafufuze za Mtumiki swallallahu …

Read More »