Monthly Archives: July 2025

Sunnats Ndi Aadaab Za Salaam 2

3. Njira ya Sunnat yakaperekedwe ka salaam ndi kupereka moni kwa Asilamu onse, osati achibale ake, abwenzi ake ndi amene akuwadziwa okha. Olemekezeka Abdullah bin Amr radhwiyallahu anhu akusimba kuti munthu wina adamufunsa Mtumiki Swallallahu alaihi wasallam “Kodi ndi chikhalidwe chanji ndi mChisilamu chomwe chili choyamikirika komanso chabwino?” Adayankha Mtumiki …

Read More »

Kulemekezeka kwa Sa’iid bin Zaid (Radhwiyallahu ‘anhu) pamaso pa Abdullah bin Umar (radhwiyallahu ‘anhuma)

Tsiku lina Abdullah bin Umar (Radhwiyallahu ‘anhuma) akukonzekera kupita ku Swalaah, adamva kuti amalume ake, Sa’iid bin Zaid (radhiyallahu ‘anhu) akudwala kwambiri ndipo atha kumwalira. Nkhaniyi idamufika pa nthawi yomwe adali atadzola kale (mafuta onunkhiritsa) thupi lake ndipo ali pafupi kuchoka kwawo kupita ku Swalaah ya Jumuah. Koma atamva nkhani …

Read More »

Sunnats Ndi Aadaab Za Salaam 1

1. Ukakumana ndi Msilamu nzako, mupatse salaamu. Olemekezeka Ali radhwiyallahu anhu akunena kuti Mtumiki (Swallallahu alaihi wasallam) adati: “Msilamu ali ndi ma ufulu asanu ndi umodzi pa Msilamu nzake. Akakumana naye amlonjere (ndi salamu); ngati amuitana avomere kuitana kwake; akayetsemula amupangire duwa ponena kuti. ‘Yarhamukallah’ akadwala azikamuona akamwalira aziperekeza nawo …

Read More »

Kuonongeka kwa Ummah asadafike Dajjaal

Zatchuridwa mMahadith kuti Qiyaamah isanafike, khumbo lalikulu la anthu lidzakhala kudzikundikira ndi kusonkhanitsa chuma. Anthu adzachitenga chuma ngati mfungulo ya zinthu zonse zapamwamba ndi chitonthozo, khomo la zosangalatsa zamtundu uliwonse ndi zansangulutso, ndi chida chokwaniritsira zokondweretsa za thupi ndi zilakolako za dziko. Kotero, adzapereka chilichonse kuti apeze ndipo adzachita chilichonse …

Read More »

Kulemekeza kwa Saiid bin Zaid (Radhwiyallahu ‘anhu) kumulemekeza Uthmaan (Radhwiyallahu ‘anhu)

Zanenedwa kuti nthawi ina munthu wina adadza kwa olemekezeka Saiid bin Zaid (Radhwiya-Allahu anhu) nati: “Ndili ndi chikondi chachikulu pa Ali (Radhwiya-Allahu ‘anhu) mu mtima mwanga moti sindikonda china chilichonse monga momwe ndimamukondera.” Saiid bin Zaid (Radhwiya-Allahu ‘anhu) adamuyamikira iye chifukwa cha chikondi ndi ulemu wake kwa Ali (Radhwiyallahu ‘anhu) …

Read More »

Ma Ubwino Okhudza Kupereka Salaam

Ubwino Oyambilira kupanga Salaam Olemekezeka Abdullah bun Masuud (Allah asangalale naye) akusimba kuti Rasulullah (madalitso ndi mtendere zikhale pa iye) adati: “Amene amayambilira kupereka Salaam ndi osadzitukumura.”[1] Njira Yokhanzikitsira Chikondi Olemekezeka Abu Hurairah (Allah asangalare naye) akusimba kuti Rasulullah (madalitso ndi mtendere zipite kwa iye) adati: “Simudzalowa ku Paradiso pokhapokha …

Read More »

Udindo Wapamwamba wa Olemekezeka Said bin Zaid (Radhwiya Allaahu ‘anhu) Pakati pa anthu a ku Madinah Munawwarah

M’nthawi ya khilaafah ya Olemekezeka Mu’aawiyah (Radhwiya Allahu ‘anhu) adalembera kalata Marwaan bin Hakam bwanamkubwa wake yemwe adasankhidwa ku Madinah Munawwarah pomwe adamulangiza kutenga bay’at (chikole cha chikhulupiriro) kwa anthu a ku Madinah Munawwarah m’malo mwa mwana wake, Yaziid bin Mu’aawiyah, yemwe adzakhale Khalifah m’malo mwake mwake. Mu’aawiyah (Radhwiyallahu ‘anhu) …

Read More »

Salaam

Salaam ndi moni wa Chisilamu. Monga momwe Chisilamu chimatanthauza mtendere, moni wa Chisilamu ndi moni wamtendere komanso ofalitsa uthenga wamtendere. Salaam ndi imodzi mwa zochitika zachisilamu zomwe ndi chizindikiro cha Msilamu, ndipo kufunika kwake kwatsindikitsidwa kwambiri mahadith. Olemekezeka Abdullah bin Salaam (Radhwiyallahuanhu) akuti: Mtumiki (madalitso ndi mtendere zikhale pa iye) …

Read More »

Nkhumbo lalikulu la Olemekezeka Saiid bin Zaid (Radhwiya Allaahu ‘anhu) lopereka Moyo Wake Munjira Ya Allah.

Mzinda wa Damasiko utagonjetsedwa ndi Asilamu, Abu Ubaidah (radhwiyallahu ‘anhu) mkulu wa asilikali achisilamu -anasankha Sa’iid bin Zaid (radhwiyallahu ‘anhu) kukhala kazembe wa mzinda wa Damasiko. Pambuyo pake Abu Ubaidah (Radhwiyallahu ‘anhu) adapitilira ndi gulu lake lankhondo kulowera ku Jordan. Atafika ku Yordan, anamanga msasa kumeneko ndi kuyamba kukonzekera zolimbana …

Read More »

Kutonthoza Oferedwa

13. Sizoloredwa kupita ku nyumba ya kafiri yemwe wamwalira kukapepesa mwambo wamaliro uli mkati. Koma akakhala kuti ndi kafiri oyandikana naye nyumba kapena kaafir aliyense amene wataya wachibale wake, mwachitsanzo, mwana, ukhoza kumutonthoza ndi mawu awa: أَخْلَفَ اللّه عَلَيْكَ خَيْرًا مِنْهُوَاَصْلَحَكَ Akhlafa Allahu ‘Alayka Khayran Minhu Wa ‘Aslahaka Allah akupatse …

Read More »