1. Valani moyenera pamene mukupita kumnzikiti
Allah ta’ala akuyankhula kuti: Oh Inu ana Aadam (alyhi salaam), zikongoleseni (valani zovala zozikongoletsera) pamene mukupemphera swalah munzikiti
Read More »1. Valani moyenera pamene mukupita kumnzikiti
Allah ta’ala akuyankhula kuti: Oh Inu ana Aadam (alyhi salaam), zikongoleseni (valani zovala zozikongoletsera) pamene mukupemphera swalah munzikiti
Read More »Hazrat Uqbah bin Aamir radhiyallahu anhu akusimba kuti Hazrat Rasulullah adati: “Ndithu, Misikiti ili ndi zikhomo (omwe ndi anthu odzipereka ku musjid, ochita ibaadah, monga ngati zikhomo zimakhomeredwa pansi). anthu oterowo, ngati atachoka ku Musjid, angelo amawasowa, ndipo ngati ali odwala, angelo amawachezetsa, ndipo angelo akawaona amawalandira, ndipo ngati angafunike, angelo amawathandiza kukwaniritsa zosowa zawo (Pamene ali (m’Msikiti kukumbukira Allah), kuwerenga kwa Duroud ndi zina zotero), Angelo amawazungulira kuyambira Kumiyendo yawo mpaka Kumwamba. Manja awo amene akulembera Duruud (yomwe ikuwerengedwa ndi anthu awa) Wonjezerani (zikr ndi Duruud) Allah akuonjezereni (zabwino)!” Pamene anthu awa ayamba kupanga zikr ya Allah, makomo akumwamba amatsekulidwa kwa iwo, mapemphelo awo amayankhidwa, anamwali aku Jannah akusuzumira pansi pawo, ndipo Allah amawaikira Chifundo Chake chapadera pokhapokha ngati Sachita china chilichonse, ndipo sakuchoka. Akachoka munzikiti , angelo amadzuka ndi kufunafuna Misonkhano ina ya zikr.
Read More »Sayyiduna Anas (radhiyallahu anhu) akusimba kuti Mtumiki sallallahu alaih wasallam adati pali gulu la Angelo la Allah lomwe limazungulira dziko lonse lapansi kuyang'anaya yang'ana gulu la anthu omwe akupanga Dhikr, akakumana ndi gulu lachoncholo amalizungukira akatero amatumiza gulu lina la Angelo kupita kumwamba kukamudziwitsa Allah zomwe anthuwa akuchitazi, angelowa amauza Allah kuti "oh Allah, takumana ndi gulu la akapolo anu omwe akuutenga mtendere wanu kukhala chinthu chapamwamba kwambiri, a kuwerenga bukhu lanu, a kumuwerengera Durood Mtumiki wanu ndipo akukupemphani zosowa zawo za padziko lapansi komanso ku Aakhirah".Allah amayankha ndikunena kuti, akutileni mu chifundo changa"ndipo angelowa amachita chomwecho ndipo amapitiliza kunena mgululi muli uje ndi uje, amene ndi ochimwa kwambiri, komanso wangobwera kumapeto kwa zonse "Allah amayankha kuti, akutileni anthu onse mchifundo changa kuphatikizapo iyeyo popeza wina aliyense amene anakutiridwa mgululi alibe tsoka lirilonse komanso samanidwa chisomo changa."
Read More »Pamene nthaka idzagwedezedwe kugwedezedwa kwenikweni. Ndipamene nthaka idzatuluse mitolo yake. ndipo munthu adzati; ´´Kodi nthaka Yatani? ``. Patsikulo limeneli nthaka idzaulula nkhani zake, Chifukwa choti Mbuye wake adzayiwuza kuti Itero. Patsiku limeneli anthu adzapita kumalo achiweruzo ali mmagulumagulu kukaonetsa ntchito zawo. Choncho amene angachite ntchito yabwino yolemera ngati njere yampiru adzaiwona. Ndipo amene angagwire ntchito yoipa yolemera ngati njere yampiru adzayiwona.
Read More »Sayyiduna Ammaar (radhiyallahu anhu) kuti Mtumiki (sallallahu alaih wasallam) adati, Allah adasankha mngelo amene amakhala pafupi ndi manda anga kuti adzindifikitsira Durood ya Ummah wanga ndipo adawazindikiritsa maina (ma hadith ena amanena kuti adapatsidwa mphamvu yozindikira mawu a anthu osiyanasiyana) zomwe zikutanthauza kuti palibe munthu amene angandiwelengere Durood tsiku lina lirilonse mpaka pa Qiyaamah pokhapokha mngeloyu amafikitsa kwa ine dzina la munthuyo komanso la bambo ake. (Amanena kuti) uyu ndi uje mwana uje amene wakuwerengerani Durood.
Read More »4. Kupitapita kumzikiti ndi njira yokhayo yomwe ingateteze Dini ya munthu.
Sayyiduna Mu’adh bin Jabal (radhiyallahu anhu) akusimba kuti Mtumiki (sallallahu alaih wasallam) adati, ndithudi satana ndi nkhandwe ya munthu (yomwe imansaka munthu kuti idye) monga m'mene nkhandwe ya ziweto imachitira yomwe imapezelera mbuzi yomwe ili yokhayokha, Pewani kukhala panokhanokha (kapena kutsata maganizo a okha) ndipo gwiritsitsani gulu la Ahlus-sunnah wal jamaa'ah ndikukhala limodzi ndi ummah komanso kulumikizana ndi mzikiti".
Read More »Sayyiduna Abdullah bin Masuud (radhiyallahu anhu) akusimba kuti Mtumiki (sallallahu alaih wasallam) adati, "ndithu Allah ali ndi gulu la Angelo lomwe limazungulira dziko lonse lapansi kuyang'anaya yang'ana duruud ya ummah wanga ndipo amaifikitsa kwa ine."
Read More »1. Kupangira wudhu kunyumba komanso Kuyenda kupita kunzikiti ndi njira yokhululukidwa machimo ndikukwezedwa ulemelero.
Sayyiduna Abu Hurairah (radhiyallahu anhu) akufotokoza kuti Mtumiki (sallallahu alaih wasallam) adati: Munthu amene angapange wudhu kunyumba ndi Kuyenda wapansi kupita kunzikiti kuti akakwaniritse lamulo la Allah phanzi lirilonse lomwe angaponye amakhulukidwa machimo, ndipo phanzi lina lomwe angaponye adzakwezedwa ulemelero wake.
Read More »
Anthu okanira mwa eni bukhu komanso ma Mushrikiin (opembedza mafano) sadafune kusiyana ndi umbuli wawo komanso zikhalidwe zawo kufikira chisonyezo chidawafikira amene ndi Mtumiki wa Allah kwawerengera makalata oyeretsedwa. M'mene mukupezeka malamulo olongosoredwa mom eka bwino. Omwe adapatsidwa mabukhu sadalekane/sadasemphane ndikugawanikana kufikira pomwe zisonyezo zoonekera poyera zidawadzera. Ndipo adangolamuridwa kumpembedza Allah kuchokera pansi pa mtima kukupanga kupembedza kukhala kwa Allah yekha osamphatikiza ndi zina. Ndikuswali komanso kupeleka Zakaat nthawi zonse ndikuti imeneyo ndiye dini yoongoka komanso.
Read More »Hazrat Abu Talhah (radhiyallahu anhu) akusimba kuti: Tsiku lina m'mawa, Mtumiki (sallallahu alaih wasallam) adabwera kwa ife ali wosangalala, mpaka chisangalalo chake chinawala kuchokera ku nkhope yake yodalitsika. Swahabah wina adafunsa: "E, Mtumiki (sallallahu alaih wasallam)! Taona kuti lero mwakondwa kwambiri. Chisangalalocho chikuwoneka bwino pa nkhope yanu yodalitsika."Mtumiki (sallallahu alaih wasallam ) adayankha: "Inde, Mtumiki wochokera kwa Mbuye wanga anabwera ndi uthenga wonena kuti: " Munthu Amene adzakuwerengere Durood mwa ummah wako kamodzi, Allah adzamulembera zabwino khumi, ndi kufafaniza ndi kukhululukira machimo ake okwana khumi, ndi kukweza udindo wake ku Jannah m’magawo khumi, ndikumuyankha Duruud yake mofanananso (ndiye kuti Allah amutumizira chifundo ndi madalitso khumi).
Read More »