admin

Malangizo Kwa Amene Amanyalanyaza Swalaah Ya Pagulu Jamaat Mu Mzikiti

Lidali khumbo la Mtumiki (swallallahu alaih wasallam) kuti amuna onse a Ummah wake adzipempelera swalah zawo ku mzikiti pa jamaa Mtumiki (swallallahu alaih wasallam) ankakhudzidwa kwambiri akazindikira kuti munthu wina wake wapemphelera kunyumba ndipo adati: “Pakadapanda kupezeka kwa akazi ndi ana, ndikadalamula gulu la achinyamata kuti lisonkhanitse nkhuni ndi kuyatsa …

Read More »

Olemekezeka Talhah (radhwiyallahu anhu) pa nkhondo ya Uhud

Olemekezeka Zubair bin Awwaam (radhwiyallahu anhu) akufotokoza kuti pa nkhondo ya Uhud Mtumiki (swallallahu alaih wasallam) adaphatikiza zovala zozitetezera pa nkhondo. Mkatikati mwa nkhondo Mtumiki (swallallahu alaih wasallam) adafuna kukwera miyala ikulu ikulu koma ankakanika chifukwa chakulemera kwa zovala za pa nkhondo.Choncho adamupempha Olemekezeka Talha (radhwiyallahu anhu) kuti akhale pansi …

Read More »

Nthawi Yoyenera Ndi Kachitidwe Koyenera

Monga momwe Swalah ilili yofunika, kuiswali mu nthawi yoyenera komanso moyenera ndikofunikanso. Sayyiduna Mtumiki (Swallallahu alaih wasallam) adati: “Munthu akapemphera Swalaah mu nthawi yake yoikika ndi wudhu woyenerera, kukwaniritsa qiyaam (kuimirira), rukuu ndi sajdah m’njira yolondora ndi mlingo wofunika okhazikika ndi kudzipereka, kenako Swala imadzuka mowala bwino ndikumuuza kuti: Allah …

Read More »

Chikondi chopanda malire cha maswahabah pa Mtumiki (swallallahu alaih wasallam)

Munthu wina adabwera kwa Mtumiki (swallallahu alaih wasallam) nati, Oh Mtumiki wa Allah (swallallahu alaih wasallam) chikondi changa pa inu chili ponena kuti ndikangokuganizani ndimazadzidwa ndi chikondi chopanda malire, ndipo mtima wanga siumakhala mmalo pokhapokha ndikuoneni, Oh Mthenga wa Allah, maganizo amandifika kuti ngati Allah anganditenge ndikukandilowetsa ku Jannah zidzakhala zovuta kwa ine kuti ndidzakuoneni popeza inu mudzakhala Jannah ya pamwamba kwambiri yomwe ine sindingakwanitse kuifika.

Read More »

Kuwerenga Durood M’malo Omwe Anthu Amanyaranyaza

عن أبي وائل قال : ما شهد عبد الله مجمعا ولا مأدبة فيقوم حتى يحمد الله ويصلي على النبي صلى الله عليه وسلم وإن كان مما يتبع أغفل مكان في السوق فيجلس فيه فيحمد الله ويصلي على النبي صلى الله عليه وسلم (المصنف لابن أبي شيبة، الرقم: 30429، ورواته ثقات) …

Read More »

Salaah Ya Amuna

Udindo wapamwamba womwe Swalah ili nawo m’moyo wa Msilamu siufunikira kufotokoza kulikonse. Mfundo yoti idzakhala gawo loyamba lomwe adzafunsidwe munthu pa tsiku la Qiyaamah ndi umboni wokwanira wotsimikizira kufunika kwake. Sayyiduna Rasulullah (swallallahu alaih wasallam) إن أول ما يحاسب الناس به يوم القيامة من أعمالهم الصلاة قال يقول ربنا جل …

Read More »

Chikondi Cha Sahabah wina pa Mtumiki (sallallahu alaih wasallam)

Sahabah wina adabwera kwa Mtumiki (sallallahu alaih wasallam) ndikufuna kuti oh Mthenga wa Allah kodi Qiyamah idzafika liti? Mtumiki (sallallahu alaih wasallam) adayankha pomufunsa kuti ndichani chomwe wachita sochinyeza kuikonzekera tsikulo? Sahabah adayankha nati, Oh Mthenga wa Allah sindikudzitenga kuti ndiri ndi swalah Saum kapena sadaqah zochuluka zomwe ndapanga komanso …

Read More »

Tafseer Ya Surah Feel

Kodi siudaone momwe Mbuye wako adawachitira anthu a Njovu? Kodi sadawaononge chiwembu chawo? Ndipo adawatumizira magulu ambalame mmagulumagulu otsatizana, ndikumawagenda ndi miyala yamoto; ndipo adawachita kukhala ngati mmera otafunidwatafunidwa ndiye walavuridwa.

Read More »

Machimo a Zaka Makumi asanu ndi atatu Akhululukidwa, sawabu za Zaka Makumi asanu ndi atatu Zilembedwa Kupyolera mu Kubwereza Durood Makumi asanu ndi atatu tsiku Lachisanu

Hazrat Abu Hurairah (radhwiyallahu anhu) akufotokoza kuti Hazrat Rasulullah (swallallahu alaih wasallam) adati "kundiwerengera Duruud kudzakhala kuwala pa Mlatho (Paul-Siraat) ndipo amene adzandiwerengere Duruud tsiku lachisanu kokwana makumi asanu ndi atatu (80), adzakhululukidwa zaka makumi asanu ndi atatu za machimo ake."

Read More »

Sunna Za Msikiti

37. Ulumikizitseni mtima wanu nthawi zonse ndiku mzikiti. Mwachitsanzo pamene mukuchoka mumzikiti pomwe mwatsiriza swalah yanu, pangani niya kuti mubweranso kumzikitiko paswala yotsatirayo ndipo idikireni swalayo ndimtima onse.[1] عن أبي هريرة رضي الله عنه أن رسول الله صلى الله عليه وسلم قال ألا أدلكم على ما يمحو الله به الخطايا …

Read More »